Jeremiah 48:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Amene akuthaŵa, amaima pa mthunzi wa Hesiboni, chifukwa chotopa kwambiri. Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni, malaŵi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni, ndipo motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu, dziko la anthu andeu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka m'Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamtu pa ana a phokoso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesiboni chifukwa chotopa. Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni, malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni. Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu, dziko la anthu onyada.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pa mthunzi wa Hesiboni; pakuti moto waturuka m'Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngondya ya Moabu, ndi pakati pamtu pa ana a phokoso,