Jeremiah 48:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Woononga uja adzasakaza mzinda uliwonse, palibe mzinda ndi umodzi womwe umene udzapulumuke. Malo am'zigwa adzaonongeka, malo okwera nawonso adzasakazika. Zidzachitika monga momwe Chauta adanenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uliwonse; chigwa chomwe chidzasakazidwa, ndipo chidikha chidzaonongedwa; monga wanena Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse, ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke. Chigwa chidzasanduka bwinja ndipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwa monga Yehova wayankhulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uli wonse; cigwa comwe cidzasakazidwa, ndipo cidikha cidzaonongedwa; monga wanena Yehova.