Jeremiah 49:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Za Aamoni, Chauta akufunsa kuti, “Kodi Israele alibe ana aamuna? Kodi alibe mloŵachuma? Chifukwa chiyani tsono anthu opembedza Milikomu alanda dziko la Gadi, ndipo akukhala m'mizinda yake?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana amuna? Alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m'midzi mwake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova ananena izi: Amoni, “Kodi Israeli alibe ana aamuna? Kapena alibe mlowamʼmalo? Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi? Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israyeli alibe ana amuna? alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi cifukwa canji, ndi anthu ace akhala m'midzi mwace?