Jeremiah 49:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ine ndachotseratu chuma chonse cha zidzukulu za Esau. Ndaonetsa poyera malo ao obisalamo, alibenso poti angabisale. Ana ao, abale ao ndi anansi ao omwe aonongeka. Palibe wina amene watsalako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndamvula Esau, ndamvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zake zaonongeka, ndi abale ake, ndi anansi ake, ndipo palibe iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ine ndazivula zidzukulu za Esau. Ndaonetsa poyera malo awo obisalamo, kotero kuti sadzathanso kubisala. Ana ake, abale ake pamodzi ndi anansi ake awonongeka. Palibe wonena kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndambvula Esau, ndambvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zace zaonongeka, ndi abale ace, ndi anansi ace, ndipo palibe iye.