Jeremiah 49:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Ngati amene sanali oyenera kumwa chikho cha chilango adzamwe ndithu, nanji inu, muyesa mudzakhala osalangidwa? Pepani, mudzalangidwa ndithu, ndipo mudzamwadi chikhocho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwe kuti amwe chikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? Sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Ngati iwo amene sanali oyenera kulangidwa adzamwa chikho cha chiweruzo, ndiye muyesa kuti inuyo simudzalangidwa? Ayi ndithu simudzakhala osalangidwa. Mudzamwa ndithu chikhocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwa kuti amwe cikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi.