Jeremiah 49:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pali Ine ndemwe, mzinda wa Bozira udzasanduka chinthu chochititsa nyansi, chomachiseka, chopanda kanthu ndi chotembereredwa. Ndipo midzi yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndalumbira, Pali Ine ati Yehova, kuti Bozira adzakhala chizizwitso, chitonzo, chopasuka, ndi chitemberero; ndipo midzi yake yonse idzakhala yopasuka chipasukire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndalumbira, Pali Ine, ati Yehova, kuti Boma adzakhala cizizwitso, citonzo, copasuka, ndi citemberero; ndipo midzi yace yonse idzakhala yopasuka cipasukire.