Jeremiah 49:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndamva uthenga wochokera kwa Chauta wamthenga watumidwa kwa anthu a mitundu ina. Akufuula kuti, “Sonkhanani pamodzi kuti mumenyane ndi Edomu, dzambatukani mukonzekere nkhondo!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndamva mthenga wa kwa Yehova, ndipo mthenga watumidwa mwa amitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova: Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti, “Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu! Konzekerani nkhondo!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndamva mthenga wa kwa Yehoya, ndipo mthenga watumidwa mwa amitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.