Jeremiah 49:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunyada kwako kwakunyenga, kuwopseza kwako kwakusokeza, iwe wokhala m'mapanga ndi m'matanthwe, ku mapiri. Ngakhale umange chisa chako pamwambamwamba ngati nkhwazi, ndidzakutsitsabe pamenepo,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuopseza kwako kwakunyenga; kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa, iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri. Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga, ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma za kuopsya kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa citunda, ngakhale usanja cisanja cako pamwamba penipeni ngati ciombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.