Jeremiah 49:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yordani umaopsera khola la nkhosa lotetezedwa bwino, Inenso mwadzidzidzi ndidzapirikitsira Aedomu kutali ndi kwao. Pambuyo pake ndidzaŵaikira woŵalamulira amene ndidzamufune Ine. Nanga ndani angafanefane ndi Ine? Ndani angandipititse kubwalo lamilandu? Ndi mtsogoleri uti amene angalimbike pamaso panga?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani kupita ku malo a msipu wobiriwira, Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo. Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine. Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani? Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wocokera ku Yordano wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amcokere; ndipo ali yense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wace, pakuti wakunga Ine ndani? adzandiikira nthawi ndani? ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?