Jeremiah 49:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipotu nthaŵi ikudza, pamene ndidzamveketse mfuu wankhondo ku Raba, likulu la ku Amoni. Mzinda umenewo udzasanduka bwinja lopanda anthu, ndipo midzi yake idzapserera. Tsono Israele adzaŵalanda zao adaniwo amene adamulanda zake,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo ana ake akazi adzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israele adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo ku Raba, likulu la Amoni; ndipo malo awo opembedzera milungu yawo adzatenthedwa ndi moto. Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mpfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo ana ace akazi adzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israyeli adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.