Jeremiah 49:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake imvani, zimene Ine Chauta ndakonza zolangira Edomu, ndiponso zolinga zake zolangira anthu a ku Temani ndi izi: Ana ao omwe adzatengedwa ndithu, ndipo anthu onse adzada nalo nkhaŵa tsoka lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala m'Temani, ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani. Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala m'Temani, ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.