Jeremiah 49:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu mtundu wina udzachita kuuluka nkudzagwera Bozira ngati nkhwazi ya mapiko otambalitsa. Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu idzakhala ili thithithi ndi mantha, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, adzafika nadzauluka ngati chiombankhanga, adzatambasulira Bozira mapiko ake, ndipo tsiku lomwemo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake. Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu idzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, adzafika nadzauluka ngati ciombankhanga, adzatambasulira Boma mapiko ace, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.