Jeremiah 49:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Za Damasiko Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu a ku Hamati ndi ku Aripadi asokonezeka, chifukwa adamva uthenga woipa. Mtima wao wachita kuti phwi ndi mantha, ndi osakhazikika ngati nyanja yosatha kukhala bata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa: “Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita mantha chifukwa amva nkhani yoyipa. Mitima yawo yagwidwa ndi mantha ndipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, cifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala cete.