Jeremiah 49:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Damasiko wataya mtima, akufuna kuthaŵa chifukwa chogwidwa ndi mantha aakulu. Akumva nkhaŵa ndi zoŵaŵa zonga za mkazi pa nthaŵi yake yochira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zovuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Damasiko alefuka. Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawa chifukwa agwidwa ndi mantha aakulu. Ali ndi nkhawa komanso mantha ngati za mayi pa nthawi yake yochira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zobvuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala.