Jeremiah 49:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za Kedara ndi za maufumu a ku Hazori amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adagonjetsa, Chauta akunena kuti, “Nyamukani mukaŵathire nkhondo ku Kedara! Aonongeni anthu akuvumawo!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a ku m'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa: “Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara. Kawonongeni anthu a kummawako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo. Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a kum'mawa.