Jeremiah 49:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gwetsani mahema ao ndipo mulande nkhosa zao. Tengani nsalu ndi katundu wao yense m'mahemamo. Landaninso ngamira zao. Anthu adzafuula kwa iwo kuti, ‘Pali zoopsa pa mbali zonsezonse!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsalu zochingira zao, ndi katundu wao yense, ndi ngamira zao; ndipo adzafuulira iwo, Mantha ponseponse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Landani matenti awo ndi nkhosa zawo, ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo. Mutengenso ngamira zawo. Anthu adzafuwula kwa iwo kuti, ‘Kuli zoopsa mbali zonse!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsaru zocingira zao, ndi katundu wao yense, ndi ngamila zao; ndipo adzapfuulira iwo, Mantha ponse ponse.