Jeremiah 49:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Lirani, inu a ku Hesiboni, pakuti mzinda wa Ai waonongeka. Lirani chokweza, inu ana aakazi a ku Raba. Valani ziguduli kuwonetsa chisoni, mulire, muthaŵire uku ndi uku m'kati mwa machinga. Ndithu, mulungu wanu Milikomu adzatengedwa ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndi akalonga ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana akazi a Raba, muvale chiguduli; chitani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m'ndende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika! Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba! Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu; thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga, chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana akazi a Raba, mubvale ciguduli; citani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m'ndende, ansembe ace ndi akuru ace pamodzi.