Jeremiah 49:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu anthu a ku Hazori, thaŵani, fulumirani, kabisaleni ku makwaŵa. Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, wakonzekera kuti amenyane nanu,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Thawani inu, yendani kutali, khalani mwakuya, Inu okhala m'Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Thawani mofulumira! Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,” akutero Yehova. “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu; wakonzekera zoti alimbane nanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Thawani inu, yendani kutari, khalani mwakuya, Inu okhala m'Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani.