Jeremiah 49:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nyamukani, kauthireni nkhondo mtundu wa anthuwo umene uli pa mtendere, anthu amene akuyesa kuti ali pabwino. Mzinda wao ndi wopanda zipata kapena mipiringidzo, udangokhala pawokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nyamukani, kwererani mtundu wokhala ndi mtendere, wokhala osadera nkhawa, ati Yehova, amene alibe zitseko ndi mapiringidzo, okhala pa okha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere, umene ukukhala mosatekeseka,” akutero Yehova, “mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo; anthu ake amakhala pa okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nyamukani, kwererani mtundu wokhala ndi mtendere, wokhala osadera nkhawa, ati Yehova, amene alibe zitseko ndi mipiringidzo, okhala pa okha.