Jeremiah 49:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
A ku Elamuwo ndidzaŵachititsa mantha pamaso pa adani ao ndiponso pamaso pa amene afuna kuwononga moyo wao. Ndidzaŵagwetsera mkwiyo wanga waukali. Ndidzaŵapirikitsa ndi lupanga mpaka kuŵatheratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzachititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera choipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awo komanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo. Ndidzawagwetsera mkwiyo wanga ndipo adzakhala pa mavuto,” akutero Yehova. “Ndidzawapirikitsa ndi lupanga mpaka nditawatheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzacititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera coipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha;