Jeremiah 49:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani mukunyadira zigwa zanu, inu anthu osakhulupirika, amene munkadalira chuma chanu nkumati, ‘Ndani angalimbane ndi ife?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chanji udzitamandira ndi zigwa, chigwa chako choyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira chuma chake, nati, Adza kwa ine ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani mukunyadira chigwa chanu, inu anthu osakhulupirika amene munadalira chuma chanu nʼkumati: ‘Ndani angandithire nkhondo?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa canji udzitamandira ndi zigwa, cigwa cako coyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira cuma cace, nati, Adza kwa ine ndani?