Jeremiah 5:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Thamangani uku ndi uku m'miseu ya Yerusalemu, mudziwonere nokha. Funafunani ku mabwalo ake ngati mungapezeke munthu, munthu wake wochita zolungama, wofunitsitsa zoona, kuti choncho Yerusalemu ndidzamkhululukire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu, mudzionere nokha, funafunani mʼmabwalo ake. Ngati mungapeze munthu mmodzi amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi, ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ace, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakucita zolungama, wakufuna coonadi; ndipo ndidzamkhululukira.