Jeremiah 5:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidzatuma adani kuti akaononge mizere ya mipesa yao, komabe osati kotheratu. Akasadze nthambi zake, poti anthu ameneŵa si ake a Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga, koma musakayiwononge kotheratu. Sadzani nthambi zake pakuti anthu amenewa si a Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwerani pa makoma ace nimupasule; koma musatsirize konse; cotsani nthambi zace pakuti siziri za Yehova.