Jeremiah 5:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe Israele, ndikukudzetsera mtundu wa anthu odzakuthira nkhondo, mtundu wake ndi wochokera kutali. Mtundu umenewu ndi wosagonjerapo, mtundu wakalekale, mtundu umene chilankhulo chake iwe suchidziŵa, ndipo zimene akunena, iwe sungazimvetse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Aisraeli,” Yehova akuti, “Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali, ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo, mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa, zimene akunena inu simungazimvetse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutari, inu nyumba ya Israyeli, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene cinenero cace simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.