Jeremiah 5:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzakutherani zokolola zanu ndi chakudya chanu. Adzapha ana anu aamuna ndi aakazi, adzakupheraninso nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu. Adzaononga mipesa yanu ndi mikuyu yanu. Adzagwetsa mwankhondo mizinda yanu yamalinga imene mumaidalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga midzi yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu, adzapha ana anu aamuna ndi aakazi; adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu, adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu. Ndi malupanga awo adzagwetsa mizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako amuna ndi akazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga midzi yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.