Jeremiah 5:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mukamafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta Mulungu wathu watichita zimenezi?’ Iwe Yeremiya uzidzayankha kuti, ‘Monga momwe mudasiyira Chauta, ndi kumatumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemonso ndimo m'mene inuyo muzidzatumikira anthu a m'dziko lachilendo.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala: pamene mudzati, Cifukwa canji Yehova Mulungu wathu aticitira ife zonse izi? ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yacilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko siliri lanu.