Jeremiah 5:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine Chauta ndikuti, Kodi simukuchita nane mantha? Kodi simukunjenjemera pamaso panga? Ndine amene ndidaika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire amene nyanjayo singaŵabzole. Mafunde ake, ngakhale aŵinduke bwanji, sangathe kupitirirapo. Ngakhale akokome chotani, sangathe kubzola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi simuyenera kuchita nane mantha?” Akutero Yehova. “Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga? Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo. Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo; mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi simundiopa Ine? ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mcenga cilekaniro ca nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? ndipo ngakhale mafunde ace acita gabvigabvi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.