Jeremiah 5:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadanenepo m'mitima mwao kuti, ‘Tiyeni tizimvera Chauta Mulungu wathu, amene amatipatsa mvula pa nthaŵi yake, mvula yachizimalupsa ndi yam'masika. Ndipo salephera kutipatsa nthaŵi ya kholola.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yake; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sananenepo mʼmitima mwawo kuti, ‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu. Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika. Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yace; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.