Jeremiah 5:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja mwa anthu anga muli ena achifwamba, amene amalalira anzao monga m'mene amachitira otchera mbalame. Amatcha misampha nakola anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akucha misampha; acha khwekhwe, agwira anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akucha misampha; acha khwekhwe, agwira anthu.