Jeremiah 5:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adanenepa nkukhala a matupi osalala. Ntchito zao zoipa nzopanda malire, saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye, kuti iyende bwino, ndipo sateteza amphaŵi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala. Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire; saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino, sateteza ufulu wa anthu osauka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kucita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.