Jeremiah 5:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo ndidati, “Ndi amphaŵi chabe aŵa, alibe ndi nzeru zomwe. Iwo sadziŵa njira ya Chauta, sazindikira zimene Mulungu wao akufuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena chiweruzo cha Mulungu wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe; anthu ochita zopusa. Sadziwa njira ya Yehova, sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena ciweruzo ca Mulungu wao.