Jeremiah 5:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake mkango wam'malunje udzaŵapha, mmbulu wochoka ku thengo udzaŵaononga. Kambuku adzaŵalalira pafupi ndi mizinda yao. Ndipo adzakadzula aliyense wotuluka, poti zolakwa zao nzambiri, abwereratu m'mbuyo kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha, mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga, kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawo kuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamo pakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulu ndipo abwerera mʼmbuyo kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace mkango woturuka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene aturukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa ziri zambiri, ndi mabwerero ao acuruka.