Jeremiah 5:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji pa zonsezi? Ana anu adandisiya Ine, ndipo adapembedza milungu imene siili milungu konse. Ine ndidaŵapatsa zonse zimene ankasoŵa, komabe adakonda kumachita chigololo, namapita ku nyumba za akazi adama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita? Ana anu andisiya Ine ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse. Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa, komabe iwo anachita chigololo namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Bwanji ndidzakhululukira iwe? pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anacita cigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama.