Jeremiah 50:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu Ababiloni, mudaononga anthu anga osankhidwa. Ngakhale mukondwe ndi kusangalala, ngakhale mulumphelumphe mokondwa ngati mwanawang'ombe wopuntha tirigu, ngakhale mulire monyada ngati akavalo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa mukondwa, chifukwa musekerera, inu amene mulanda cholowa changa, chifukwa muli onenepa monga ng'ombe yaikazi yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu Ababuloni, munawononga anthu anga osankhika. Ndiye pano mukukondwa, mukusangalala. Mukulumphalumpha mokondwa ngati mwana wangʼombe wopuntha tirigu ndiponso mukulira monyada ngati ngʼombe zazimuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa mukondwa, cifukwa musekerera, inu amene mulanda colowa canga, cifukwa muli onenepa monga ng'ombe yamsoti yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;