Jeremiah 50:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mzinda wanu udzachititsidwa manyazi ndithu kwambiri. Mzinda umene uli ngati mai wanu adzaunyazitsa. Ndithudi, Ababiloni adzakhala otsirizira mwa anthu a mitundu yonse. Mzinda wao udzakhala ngati thengo, ngati dziko louma lachipululu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, chipululu, dziko louma, bwinja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mzinda wanu udzachititsidwa manyazi kwambiri. Mzinda umene uli ngati mayi wanu udzanyazitsidwa. Babuloni adzasanduka chitsirizira cha anthu onse. Mzinda wawo udzakhala ngati thengo, ngati dziko lowuma lachipululu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, cipululu, dziko louma, bwinja.