Jeremiah 50:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzakhala wopanda anthu chifukwa cha mkwiyo wa Chauta, udzakhala chipululu chokhachokha. Onse odutsa ku Babiloni azidzachita nyansi, nkumangotsonya chifukwa cha mabala a mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babiloni adzadabwa, adzatsonyera pa zovuta zake zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova Babuloni adzakhala wopanda anthu ndipo adzakhala chipululu chokhachokha. Onse odutsa kumeneko adzachita mantha ndipo azidzangotsonya chifukwa cha chiwonongeko chake chachikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babulo adzadabwa, adzatsonyera pa zobvuta zace zonse.