Jeremiah 50:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Konzekani kuti mumzinge Babiloni pa mbali zonse, inu okoka mauta. Mlaseni, chulukitsani mivi yanu. Iye uja adachimwira Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Gubani ndi kuzungulira Babiloni kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mivi; pakuti wachimwira Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu okoka uta, konzekani kuti muthire nkhondo mzinda wa Babuloni mbali zonse. Muponyereni mivi yanu yonse chifukwa anachimwira Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Gubani ndi kuzungulira Babulo kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mibvi; pakuti wacimwira Yehova.