Jeremiah 50:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfuulireni ponseponse pakuti wagonja. Nsanja zake zagwa, malinga ake aonongeka. Kumeneku ndiko kulipsira kwa Chauta. Mlipsireni, mumchite zonga zomwe iye adaŵachita ena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mumfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ake agwa; makoma ake agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; mumbwezere chilango; monga iye wachita mumchitire iye momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mufuwulireni mbali zonse pakuti wagonja. Nsanja zake zagwa. Malinga ake agwetsedwa. Kumeneku ndiko kulipsira kwa Yehova. Mulipsireni, mumuchite zomwe iye anachitira anthu ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mumpfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ace agwa; makoma ace agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; mumbwezere cilango; monga iye wacita mumcitire iye momwemo.