Jeremiah 50:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku Babiloniko chotsani wofesa aliyense ndiponso aliyense wodula tirigu ndi chikwakwa chake pa nthaŵi yokolola. Poopa lupanga la ozunza anzao, aliyense adzatembenukira kwa anthu ake, nkuthaŵira ku dziko lakwao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muwathe ofesa ku Babiloni, ndi iwo amene agwira chisenga nyengo ya masika; chifukwa cha lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ake, nadzathawira yense ku dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chotsani ku Babuloni munthu wofesa mbewu aliyense, ndiponso wodula tirigu ndi chikwakwa chake pa nthawi yokolola. Poona lupanga la ozunza anzawo, aliyense adzabwerera kwa anthu ake; adzathawira ku dziko la kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muwathe ofesa ku Babulo, ndi iwo amene agwira zenga nyengo ya masika; cifukwa ca lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ace, nadzathawira yense ku dziko lace.