Jeremiah 50:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele ali ngati nkhosa zomwazika, zopirikitsidwa ndi mikango. Mfumu ya ku Asiriya ndiyo idayamba kuŵapha Aisraelewo, nkudzabwera Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni kudzachita ngati kupwepweta mafupa ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aisraeli ali ngati nkhosa zomwe zabalalika pothamangitsidwa ndi mikango. Mfumu ya ku Asiriya ndiye inayamba kuwapha Aisraeliwo. Wotsiriza anali Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni amene anachita ngati kuphwanya mafupa ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Israyeli ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampitikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asuri; ndipo pomariza Nebukadirezara uyo watyola mafupa ace.