Jeremiah 50:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndidzailanga mfumu ya ku Babiloniyo pamodzi ndi dziko lake, monga momwe ndidalangira mfumu ya ku Asiriya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni ndi dziko lake, monga ndinalanga mfumu ya Asiriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi dziko lake monga momwe ndinalangira mfumu ya ku Asiriya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzalanga mfumu ya ku Babulo ndi dziko lace, monga ndinalanga mfumu ya Asuri.