Jeremiah 50:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Israele ndidzambwezera kubusa kwake, ndipo azikadya ku Karimele ndi ku Basani. Adzadya chakudya chokwanira ku mapiri a ku Efuremu ndi ku Giliyadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzabwezeranso Israele kubusa lake, ndipo adzadya pa Karimele ndi pa Basani, moyo wake nudzakhuta pa mapiri a Efuremu ndi m'Giliyadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndidzabwezera Israeli ku msipu wake ndipo adzadya mʼminda ya ku Karimeli ndi Basani; adzadya nakhuta ku mapiri a ku Efereimu ndi Giliyadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzabwezeranso Israyeli ku busa lace, ndipo adzadya pa Karimeli ndi pa Basana, moyo wace nudzakhuta pa mapiri a Efraimu ndi m'Gileadi.