Jeremiah 50:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ulengeze ndi kulalika kwa anthu a mitundu yonse. Kweza mbendera ndipo usabise kanthu, uŵauze kuti, ‘Babiloni wagwa! Mulungu wake Beli wachititsidwa manyazi, nayenso Merodaki wataya mtima. Mafano ake anyozedwa kwambiri, milungu yake yataya mtima.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Lengeza ndi kulalika pakati pa anthu a mitundu ina, kweza mbendera ndipo ulengeze; usabise kanthu, koma uwawuze kuti, ‘Babuloni wagwa; mulungu wawo Beli wachititsidwa manyazi, nayenso Mariduku wagwidwa ndi mantha. Milungu yake yagwidwa ndi mantha ndipo mafano ake adzagwidwa ndi mantha.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babulo wagwidwa, Beli wacitidwa manyazi, Merodake watyokatyoka, zosema zace zacitidwa manyazi, mafano ace atyokatyoka.