Jeremiah 50:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku amenewo, nthaŵi imeneyi ikadzafika, adzafunafuna zolakwa za Israele, koma sichidzapezeka nchimodzi chomwe. Adzafufuzafufuza machimo a Yuda, koma silidzapezeka nlimodzi lomwe. Pakuti otsala amene ndaŵasiya aja ndidzaŵakhululukira,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masiku amenewo, nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “anthu adzafunafuna zolakwa za Israeli koma sadzapeza nʼchimodzi chomwe, ndipo adzafufuza machimo a Yuda, koma sadzapeza ndi limodzi lomwe, chifukwa otsala amene ndawasiya ndidzawakhululukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israyeli zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zocimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati cotsala.