Jeremiah 50:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene anali ngati nyundo ya dziko lapansi uja, onani m'mene aphwanyikira. Onani m'mene Babiloni wasandukira chinthu chonyansa pakati pa mitundu ya anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kuthyoka! Babiloni wasanduka bwinja pakati pa amitundu!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani mʼmene waphwanyikira ndi kuwonongekera uja amati ndi nyundo ya dziko lonse lapansi. Mzinda wa Babuloni wasanduka chinthu chochititsa mantha pakati pa mitundu ina!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kutyoka! Babulo wasandulca bwinja pakati pa amitundu!