Jeremiah 50:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe Babiloni, ndakutchera msampha ndipo wakodwamo, iwe osazindikira kanthu. Udapezeka ndipo udagwidwa chifukwa chakuti udaalimbana ndi Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndakutchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babiloni, ndipo sunadziwa, wapezeka, ndiponso wagwidwa, chifukwa walimbana ndi Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinakutchera msampha, iwe Babuloni, ndipo wakodwamo iwe wosazindikira kanthu; unapezeka ndiponso unakodwa chifukwa unalimbana ndi Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndakuchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babulo, ndipo sunadziwa, wapezeka, ndiponso wagwidwa, cifukwa walimbana ndi Yehova.