Jeremiah 50:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumenyane naye Babiloni mbali zonsezonse. Tsekulani nkhokwe zake. Anthu ake muŵaunjike ngati milu ya tirigu, ndipo muŵaononge kotheratu, pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tadzani kudzamenyana ndi iye kuchokera ku malekezero ake, tsegulani pa nkhokwe zake; unjikani zake monga miyulu, mumuononge konse; pasatsale kanthu ka pa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumenyane naye Babuloni mbali zonse. Anthu ake muwawunjike ngati milu ya tirigu. Muwawononge kotheratu ndipo pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tadzani kudzamenyana ndi iye kucokera ku malekezero ace, tsegulani pa nkhokwe zace; unjikani zace monga miyulu, mumuononge konse; pasatsale kanthu ka pa iye.