Jeremiah 50:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muitane onse oponya mivi kuti amthire nkhondo Babiloni, abwerenso onse okoka mauta. Mzingeni ndi zithando zankhondo kuti asathaŵepo munthu ndi mmodzi yemwe. Mlangeni potsata zolakwa zake. Mchiteni zomwe iye adaŵachita ena. Iyeyu adanyoza Chauta, Woyera uja wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Memezani amauta amenyane ndi Babiloni, onse amene akoka uta; mummangire iye zithando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wake yense; mumbwezere iye monga mwa ntchito yake; monga mwa zonse wazichita, mumchitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Itanani anthu oponya mivi kudzathira nkhondo Babuloni. Muyitanenso onse amene amakoka mauta. Mangani misasa ya nkhondo momuzungulira; musalole munthu aliyense kuthawa. Muchiteni monga momwe iye anachitira anthu ena. Iyeyu ananyoza Yehova, Woyera wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Memezani amauta amenyane ndi Babulo, onse amene akoka uta; mummangire iye zitando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wace yense; mumbwezere iye monga mwa nchito yace; monga mwa zonse wazicita, mumcitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israyeli.