Jeremiah 50:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu a ku Israele akuzunzidwa pamodzi ndi anthu a ku Yuda. Onse amene adaŵagwira ukapolo aŵagwiritsa, osafuna kuŵamasula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu atero. Ana a Israele ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu a ku Israeli akuzunzidwa, pamodzi ndi anthu a ku Yuda, ndipo onse amene anawagwira ukapolo awagwiritsitsa, akukana kuwamasula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu atero: Ana a Israyeli ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.