Jeremiah 50:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mpulumutsi wao ndi wamphamvu, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Adzaŵaimira pa mlandu, kuti apatse mtendere dziko lonse lapansi, koma adzavutitsa okhala ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lake Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumutse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu; dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. Iye adzawateteza molimba pa mlandu wawo nʼcholinga choti abweretse mtendere mʼdziko lawo, koma adzavutitsa okhala ku Babuloni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lace Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumitse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babulo.